Psalms 50

Salimo la Asafu.

1Wamphamvuyo, Yehova Mulungu,
akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi
kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
2Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri
Mulungu akuwala.
3Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete;
moto ukunyeketsa patsogolo pake,
ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
4Iye akuyitanitsa zamumlengalenga
ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
5Mundisonkhanitsire okhulupirika anga,
amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
6Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake,
pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.

7Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula,
iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa;
ndine Mulungu, Mulungu wako.
8Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako,
kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.
9Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako
kapena mbuzi za mʼkhola lako,
10pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga
ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.
11Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri
ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.
12Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani,
pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.
13Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna
kapena kumwa magazi a mbuzi?
14“Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu,
kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.
15Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso;
Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”
16Koma kwa woyipa, Mulungu akuti,

“Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga
kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?
17Iwe umadana ndi malangizo anga
ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.
18Ukaona wakuba umamutsatira,
umachita maere ako pamodzi ndi achigololo
19Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa
ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.
20Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako
ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.
21Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete;
umaganiza kuti ndine wofanana nawe
koma ndidzakudzudzula
ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.

22“Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu
kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
23Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza,
ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse
chipulumutso cha Mulungu.”
Copyright information for NyaCCL